25 Pamenepo Davide anauza mthengayo kuti: “Ukamuuze Yowabu kuti, ‘Usavutike mtima chifukwa cha nkhani imeneyi, pakuti lupanga lingakanthe+ wina aliyense. Inuyo menyani nkhondo mwamphamvu ndi mzindawo ndipo muugonjetse.’+ Choncho, ukamulimbikitse Yowabu.”