2 Atatero, Davide anagawa anthuwo m’magulu atatu.+ Gulu loyamba analipereka kwa Yowabu,+ gulu lachiwiri analipereka kwa Abisai+ mwana wa Zeruya, m’bale wake wa Yowabu,+ ndipo gulu lachitatu analipereka kwa Itai+ Mgiti. Kenako mfumu inauza anthuwo kuti: “Inenso ndipita nanu sindilephera.”