21 Ndiyeno atumiki a Abisalomu atachoka, Ahimazi ndi Yonatani anatuluka m’chitsimemo ndi kupita kukauza Mfumu Davide kuti: “Anthu inu nyamukani mwamsanga muwoloke mtsinje, pakuti Ahitofeli wapereka malangizo+ ndipo wanena zakutizakuti kuti athane nanu.”