2 Tsopano nyumba ya Sauli inali ndi mtumiki, dzina lake Ziba.+ Choncho anamuitanira kwa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Ziba?” Iye anayankha kuti: “Inde, ndine mtumiki wanu.”
9 Ndiyeno mfumu inaitana Ziba, mtumiki wa Sauli, ndi kumuuza kuti: “Chilichonse chimene chinali cha Sauli komanso chilichonse cha m’nyumba yake yonse, ine ndikupereka+ kwa mdzukulu wa mbuye wako.