-
1 Mbiri 12:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Ndiyeno panali Agadi ena amene anasankha kupita kumbali ya Davide m’chipululu,+ kumalo ovuta kufikako. Amenewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima, asilikali okonzekera nkhondo, amene zishango zawo zazikulu ndi mikondo yawo ing’onoing’ono zinkakhala zokonzeka.+ Nkhope zawo zinali ngati nkhope za mikango,+ ndipo liwiro lawo linali ngati la mbawala m’mapiri.+
-