16 Davide atakweza maso ake, anaona mngelo wa Yehova+ ataima m’malere, pakati padziko lapansi ndi kumwamba. Mngeloyo anali atagwira lupanga+ n’kuloza nalo Yerusalemu. Nthawi yomweyo, Davide ndi akulu amene anali naye, atavala ziguduli,+ anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+