14 Iyo inayamba kulankhula kwa anthuwo motsatira malangizo amene achinyamata aja anaipatsa.+ Inati: “Ine ndidzakusenzetsani goli lolemera kwambiri, ndipo ndidzawonjezera goli lanulo. Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu, koma ine ndidzakukwapulani ndi zikoti zaminga.”+