17 Kenako iye anati: “Kodi chipilala chimene ndikuchiona apocho n’cha chiyani?” Pamenepo amuna a mumzindawo anamuyankha kuti: “Ndi manda+ a munthu wa Mulungu woona amene anachokera ku Yuda,+ n’kulengeza zinthu zotsutsa guwa lansembe la ku Beteli, zimene mwachita inuzi.”+