15 Kenako iye pamodzi ndi gulu lake lonse anabwerera kwa munthu wa Mulungu woona+ uja. Anaima pamaso pake n’kunena kuti: “Tsopano ndadziwa ndithu kuti, padziko lonse lapansi kulibenso kwina kumene kuli Mulungu kupatula ku Isiraeli kokha.+ Ndiye landirani mphatso+ kuchokera kwa ine mtumiki wanu.”