8 ndipo ndinang’amba+ ufumuwo kuuchotsa kunyumba ya Davide ndi kuupereka kwa iwe, koma iwe sunakhale ngati Davide mtumiki wanga. Iyeyo anasunga malamulo anga ndi kunditsatira ndi mtima wake wonse mwa kuchita zinthu zoyenera zokhazokha m’maso mwanga.+