Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 9:54
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 54 Msangamsanga Abimeleki anaitana mtumiki wake womunyamulira zida ndi kumuuza kuti: “Tenga lupanga lako undiphe,+ kuopera kuti anthu anganene za ine kuti, ‘Anaphedwa ndi mkazi.’” Nthawi yomweyo, mtumiki wakeyo anamubaya* ndi lupanga, ndipo anafa.+

  • 1 Samueli 31:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako+ undibaye* nalo, kuti amuna osadulidwawa+ asandipeze ndi kundibaya komanso kundizunza.” Koma womunyamulira zida uja sanafune,+ chifukwa anali kuopa kwambiri. Chotero Sauli anatenga lupanga lake ndi kuligwera.+

  • 2 Samueli 17:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Koma Ahitofeli ataona kuti malangizo ake sanawagwiritse ntchito,+ anakwera bulu wake ndi kunyamuka kupita kunyumba yake kumzinda wakwawo.+ Kenako anakonzekeretsa banja lake+ ndipo anadzimangirira+ moti anafa.+ Chotero anaikidwa m’manda+ a makolo ake.

  • Mateyu 27:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Choncho iye anaponya ndalama zasiliva zija m’kachisi n’kuchoka, ndipo anakadzimangirira.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena