Ekisodo 22:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 “Usatemberere Mulungu+ kapena kutemberera mtsogoleri amene ali pakati pa anthu ako.+ Levitiko 24:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Wonyoza dzina la Yehova aziphedwa ndithu.+ Khamu lonse lizim’ponya miyala. Kaya ndi mlendo wokhala pakati panu kapena nzika, aziphedwa chifukwa chonyoza Dzinalo.+ Mateyu 26:65 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 65 Pamenepo mkulu wa ansembe anang’amba malaya ake akunja n’kunena kuti: “Wanyoza Mulungu!+ Nanga n’kufunanso mboni zina pamenepa?+ Pano mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu.+ Machitidwe 23:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Pamenepo Paulo anati: “Abale, sindinadziwe kuti ndi mkulu wa ansembe. Pakuti Malemba amati, ‘Wolamulira wa anthu a mtundu wako usamunenere zachipongwe.’”+
16 Wonyoza dzina la Yehova aziphedwa ndithu.+ Khamu lonse lizim’ponya miyala. Kaya ndi mlendo wokhala pakati panu kapena nzika, aziphedwa chifukwa chonyoza Dzinalo.+
65 Pamenepo mkulu wa ansembe anang’amba malaya ake akunja n’kunena kuti: “Wanyoza Mulungu!+ Nanga n’kufunanso mboni zina pamenepa?+ Pano mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu.+
5 Pamenepo Paulo anati: “Abale, sindinadziwe kuti ndi mkulu wa ansembe. Pakuti Malemba amati, ‘Wolamulira wa anthu a mtundu wako usamunenere zachipongwe.’”+