5 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+
8 Nyumba yonse ya Ahabu+ ifafanizidwe. Ine ndidzapha munthu aliyense wokodzera khoma*+ wa m’banja la Ahabu, ngakhale aliyense wonyozeka ndi wopanda pake+ mu Isiraeli.
7 Anthuwo atangolandira kalatayo, anatenga ana aamuna a mfumu okwanira 70 aja+ n’kuwapha. Kenako anatenga mitu yawo n’kuiika m’madengu, ndipo anaitumiza kwa Yehu ku Yezereeli.