31 Ndiyeno atumiki ake anamuuza kuti: “Tamva kuti mafumu a nyumba ya Isiraeli ndiwo mafumu amene amasonyeza kukoma mtima kosatha.+ Tiyeni tivale ziguduli+ m’chiuno mwathu+ ndi kumanga zingwe kumutu kwathu, kuti tipite kwa mfumu ya Isiraeli. Mwina sikakuphani.”+