8 Mayina a amuna amphamvu+ a Davide ndi awa: Yosebu-basebete+ Mtahakemoni, mtsogoleri wa amuna atatu. Iye anatenga mkondo wake n’kupha anthu 800 ulendo umodzi.
10 Tsopano otsatirawa ndiwo atsogoleri a amuna amphamvu+ a Davide omwe anali kulimbikitsa nawo ufumu wake mwamphamvu pamodzi ndi Aisiraeli onse, kuti iye akhale mfumu malinga ndi mawu a Yehova+ okhudza Isiraeli.