Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 43:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Tsopano Yosefe anachokapo mofulumira chifukwa anagwidwa chifundo mumtima poona m’bale wakeyo.+ Anafunafuna malo oti akalirire, ndipo analowa m’chipinda chamkati n’kukagwetsa misozi.+

  • Yesaya 49:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa, osamvera chisoni mwana wochokera m’mimba mwake?+ Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiwala,+ koma ine sindidzakuiwala.+

  • Yeremiya 31:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Kodi Efuraimu si mwana wanga wamtengo wapatali, kapena mwana wanga wokondedwa?+ Pamlingo umene ndalankhula zomulanga, ndidzakumbukira kumuchitira zabwino pamlingo womwewo.+ N’chifukwa chake m’mimba mwanga mukubwadamuka chifukwa cha iye.+ Mosalephera ndidzamumvera chisoni,”+ watero Yehova.

  • Hoseya 11:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Kodi ndikusiyirenji iwe Efuraimu?+ Kodi ndikuperekerenji kwa adani iwe Isiraeli?+ Kodi ndikusandutsirenji ngati Adima?+ Kodi ndikuchitirenji zofanana ndi zimene ndinachitira Zeboyimu?+ Mtima wanga wasintha+ ndipo pa nthawi imodzimodziyo wadzaza ndi chisoni.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena