56 Ndipo mkazi wolobodoka nkhongono ndi wachisasati pakati panu, amene sanayesepo n’komwe kupondetsa phazi lake pansi chifukwa cha kuleredwa mwachisasati ndi kulobodoka nkhongono,+ ameneyu adzayang’ana ndi diso loipa mwamuna wake wokondedwa, mwana wake wamwamuna ndi mwana wake wamkazi.