Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:53
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 53 Pamenepo udzadya chipatso cha mimba yako, mnofu wa ana ako aamuna ndi ana ako aakazi,+ amene Yehova Mulungu wako wakupatsa, chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene adani ako adzakupanikiza nazo.

  • 2 Mafumu 6:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Choncho tinaphika+ mwana wanga n’kumudya.+ Tsiku lotsatira ndinauza mayiyu kuti, ‘Bweretsa mwana wako timudye.’ Koma iye anakam’bisa.”

  • Yeremiya 19:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndidzawachititsa kudya mnofu wa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. Aliyense adzadya mnzake, chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene adani awo ndiponso anthu amene akufuna moyo wawo adzawapanikiza nazo.”’+

  • Maliro 2:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Inu Yehova, yang’anani kuti muone+ yemwe mwamulanga chotere.

      Kodi amayi azidya zipatso za mimba yawo, ana awo athanzi?+

      Kapena kodi wansembe ndi mneneri aziphedwa m’malo opatulika a Yehova?+

  • Maliro 4:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ngakhale amayi, amene amakhala achifundo, afika pophika ana awo ndi manja awo.+

      Anawo akhala ngati chakudya chotonthoza anthu pa nthawi ya kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+

  • Ezekieli 5:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “‘“Choncho pakati pako, abambo adzadya ana awo+ ndipo ana adzadya abambo awo. Ine ndidzakulanga ndipo anthu ako onse otsala ndidzawabalalitsira kumphepo zonse zinayi.”’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena