-
2 Mbiri 2:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ameneyu ndi mwana wa mayi winawake wa fuko la Dani, koma bambo ake anali a ku Turo. Iye ndi wodziwa ntchito zagolide, zasiliva, zamkuwa,+ zachitsulo, zamiyala,+ ndi zamatabwa. Amadziwanso ntchito za ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira+ ndi utoto wabuluu,+ komanso ntchito za nsalu+ zabwino kwambiri ndi zofiira.+ Iye amadziwanso ntchito zamtundu uliwonse zojambula ndi kulemba mochita kugoba.+ Amadziwanso ntchito zokonza zipangizo zamtundu uliwonse+ zimene angapatsidwe kuti achite pamodzi ndi anthu anu aluso ndi anthu aluso a mbuye wanga Davide bambo anu.
-