14 Mayi ake anali mkazi wamasiye wa fuko la Nafitali. Bambo ake anali a ku Turo+ odziwa kupanga zinthu ndi mkuwa.+ Hiramu anali wanzeru, womvetsa bwino zinthu,+ ndiponso wodziwa bwino kupanga zinthu zosiyanasiyana zamkuwa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomo n’kuyamba kumugwirira ntchito yake yonse.