29 Pamalata amene anali pakati pa zitsulo zopingasana anajambulapo mikango,+ ng’ombe zamphongo,+ ndi akerubi.+ Pazitsulo zopingasana anajambulaponso zimenezo mochita kugoba. Pamwamba ndi pansi pa mikango ndi ng’ombe zamphongozo, anajambulapo mochita kugoba nkhata zamaluwa+ zopendeketsa.