13 Malo okwezeka amene anali kutsogolo+ kwa Yerusalemu kudzanja lamanja la Phiri Lachiwonongeko, amene Solomo+ mfumu ya Isiraeli inamangira Asitoreti+ chonyansa cha Asidoni, Kemosi+ chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu+ chonyansa cha ana a Amoni, mfumuyo inawasandutsa osayenera kulambirako.