13 Kodi simukudziwa zimene ineyo ndi makolo anga tinachita kwa anthu onse a mayiko ena?+ Kodi milungu+ ya mitundu ya mayiko ena inatha kupulumutsa mayiko awo m’manja mwanga?
11 kodi sizidzachitika kuti monga momwe ndidzachitire kwa Samariya ndi kwa milungu yake yopanda phindu,+ ndi mmenenso ndidzachitire kwa Yerusalemu ndi kwa mafano ake?’+