9 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+
40Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya, pamene Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anamumasula ku Rama.+ Yeremiya anali womangidwa maunyolo a m’manja pamene Nebuzaradani anamutenga pakati pa anthu a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene anali kupita ku ukapolo ku Babulo.+