-
2 Mafumu 24:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Mfumuyo inatenga+ anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ amuna onse amphamvu ndi olimba mtima,+ mmisiri aliyense+ ndi munthu aliyense womanga makoma achitetezo, n’kupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu onyozeka+ okha a m’dzikolo.
-
-
Yeremiya 40:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Patapita nthawi, akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali m’madera a kunja kwa mzinda+ pamodzi ndi anthu awo, anamva kuti mfumu ya Babulo yaika Gedaliya mwana wa Ahikamu kukhala wolamulira dzikolo. Anamvanso kuti yamuika kuti azilamulira amuna, akazi, ana ndi anthu onyozeka m’dzikolo amene sanatengedwe kupita ku ukapolo ku Babulo.+
-