Ekisodo 20:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+ 1 Mafumu 19:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Ine ndasiya anthu 7,000 mu Isiraeli,+ amene mawondo awo sanagwadirepo Baala,+ ndiponso pakamwa pawo sipanapsompsonepo Baala.”+ 2 Mafumu 17:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 pamene Yehova anachita nawo pangano+ n’kuwalamula kuti: “Musamaope milungu ina.+ Musamaigwadire kapena kuitumikira kapenanso kupereka nsembe kwa iyo.+
5 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+
18 Ine ndasiya anthu 7,000 mu Isiraeli,+ amene mawondo awo sanagwadirepo Baala,+ ndiponso pakamwa pawo sipanapsompsonepo Baala.”+
35 pamene Yehova anachita nawo pangano+ n’kuwalamula kuti: “Musamaope milungu ina.+ Musamaigwadire kapena kuitumikira kapenanso kupereka nsembe kwa iyo.+