Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 20:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+

  • Ekisodo 23:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Usaweramire milungu yawo kapena kuitumikira, ndipo usapange chilichonse chofanana ndi zifaniziro zawo,+ koma uzigwetse ndithu ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+

  • Ekisodo 34:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pakuti simuyenera kugwadira mulungu wina,+ chifukwa Yehova, amene dzina lake ndi Nsanje, alidi Mulungu wansanje.*+

  • Deuteronomo 4:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “Ukakakhala ndi ana ndi zidzukulu ndipo mwakhala nthawi yaitali m’dzikomo, n’kuchita zinthu zokuwonongetsa+ mwa kupanga chifaniziro,+ chifaniziro cha chinthu chilichonse, n’kuchita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wako,+ moti n’kumulakwira,

  • Deuteronomo 5:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo,* chifukwa cha zolakwa za anthu odana ndi ine.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena