Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 14:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pamenepo Mose anauza anthuwo kuti: “Musachite mantha.+ Chilimikani ndi kuona chipulumutso cha Yehova chimene akuchitireni lero.+ Pakuti Aiguputo amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso, ndithu, simudzawaonanso.+

  • Salimo 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Sindidzaopa anthu masauzande makumimakumi

      Amene andiukira ndi kundizungulira.+

  • Salimo 11:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ine ndathawira kwa Yehova.+

      Kodi mulibe mantha? Mukundiuza kuti:

      “Thawirani kumapiri anu ngati mbalame!+

  • Salimo 18:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Yehova ndiye thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine.+

      Mulungu wanga ndiye thanthwe langa. Ine ndidzathawira kwa iye.+

      Iye ndiye chishango changa, nyanga* yanga ya chipulumutso ndiponso ndiye malo anga okwezeka achitetezo.+

  • Salimo 118:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Mitunduyo inandizungulira, ndithu inandizungulira kumbali zonse.+

      Koma ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena