9 Chongofunika n’chakuti musam’pandukire Yehova.+ Komanso anthu a m’dzikolo musawaope,+ chifukwa ali ngati chakudya kwa ife. Alibenso chitetezo,+ koma ifeyo Yehova ali nafe.+ Musawaope ayi.”+
15 Choncho Yahazieli anati: “Tamverani Ayuda nonsenu, anthu okhala mu Yerusalemu, ndi inu Mfumu Yehosafati! Izi n’zimene Yehova wanena kwa inu, ‘Musaope+ kapena kuchita mantha ndi khamu lalikululi, popeza nkhondoyi si yanu ndi ya Mulungu.+