18 Pa nkhani yotsatirayi, Yehova andikhululukire ine mtumiki wanu: Ndikakalowa m’kachisi wa Rimoni+ pamodzi ndi mbuyanga, nditam’chirikiza+ mbuyangayo pomugwira dzanja pamene akugwadira+ Rimoni, ine n’kugwada nawo m’kachisi wa Rimoni, Yehova andikhululukire ine mtumiki wanu pa nkhani imeneyi.”+