2 Ahabu anauza Naboti kuti: “Ndipatse+ munda wako wa mpesawu+ kuti ukhale munda+ wanga woti ndizilimamo masamba,+ chifukwa uli pafupi ndi nyumba yanga. M’malo mwa munda wakowu ndikupatsa munda wina wa mpesa, wabwino kuposa umenewu. Ngati ungafune,+ ndiugula ndi ndalama.”