17 “Usalakelake nyumba ya mnzako. Usalakelake mkazi wa mnzako,+ kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ng’ombe yake, bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”+
21 “‘Usalakelake mkazi wa mnzako.+ Usalakelake mwadyera nyumba ya mnzako, munda wake, kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ng’ombe yake yamphongo, bulu wake, kapena chinthu chilichonse cha mnzako.’+
9 “‘Tsoka kwa munthu amene akupezera nyumba yake phindu mwachinyengo.+ Iye akuchita zimenezi kuti amange chisa chake pamalo okwezeka ndi cholinga choti tsoka lisamupeze.+
15 Kenako anauza anthuwo kuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse,+ chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”+
14 Ali ndi maso odzaza ndi chigololo+ komanso olephera kupewa kuchita tchimo,+ ndipo amakopa anthu apendapenda. Ali ndi mtima wophunzitsidwa kusirira mwansanje.+ Iwo ndi ana otembereredwa.+