12 Nthawi yonseyi Elisa anali kuona zimene zinali kuchitikazo, ndipo anali kufuula kuti: “Bambo anga, bambo anga!+ Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera mahatchi ake!”+ Zitatero, Elisa sanamuonenso Eliya. Kenako Elisa anagwira zovala zake n’kuzing’amba pakati.+