45 “Matemberero onsewa+ adzakugwera, kukutsatira ndi kukupeza kufikira utafafanizika,+ chifukwa sunamvere mawu a Yehova Mulungu wako mwa kusunga malamulo ndi mfundo zake zimene anakupatsa.+
14 Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, wakuti: “Ndachimwa. Siyani kundiukira. Ndikupatsani chilichonse chimene mungandilamule.”+ Chotero mfumu ya Asuri inalamula Hezekiya mfumu ya Yuda kuti apereke matalente* 300 a siliva+ ndi matalente 30 a golide.