7 Chotero, akuluakulu a ku Mowabu ndi a ku Midiyani anapita kwa Balamu+ atatenga malipiro okamulipira kuti awawombezere maula,+ komanso anamuuza zimene Balaki ananena.
2 Amidiyaniwo anayamba kusautsa Aisiraeli.+ Chifukwa cha kusautsidwa ndi Amidiyani kumeneku, ana a Isiraeli anadzikonzera malo apansi osungiramo zinthu m’mapiri. Anadzikonzeranso mapanga ndi malo ena ovuta kufikako kuti azithawirako.+