5 Pa mapeto pake, Solomo anamaliza ntchito yonse ya panyumba ya Yehova imene anayenera kugwira.+ Kenako Solomo anayamba kubweretsa zinthu zimene Davide bambo ake+ anaziyeretsa. Siliva, golide, ndi ziwiya zonse anaziika mosungira chuma cha panyumba ya Mulungu woona.+