24 Atatero, anatentha ndi moto mzindawo ndi zonse zimene zinali mmenemo.+ Koma siliva, golide, zipangizo zamkuwa ndi zachitsulo, anazipereka kuti zipite ku chuma cha nyumba ya Yehova.+
11 Zinthu zimenezi Mfumu Davide inazipatulira+ Yehova pamodzi ndi siliva ndi golide amene inalanda ku mitundu yonse,+ kuchokera ku Edomu, ku Mowabu,+ kwa ana a Amoni,+ Afilisiti,+ ndi Aamaleki.+