Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yoswa 6:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Siliva, golide, ndi zipangizo zamkuwa ndi zachitsulo, zonse n’zopatulika kwa Yehova.+ Ziyenera kupita ku chuma cha Yehova.”+

  • 1 Mafumu 7:51
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 51 Pa mapeto pake, Mfumu Solomo inamaliza+ ntchito yonse yokhudza nyumba ya Yehova imene inayenera kugwira. Kenako Solomo anayamba kubweretsa zinthu zonse zimene Davide bambo ake+ anaziyeretsa. Anatenga siliva, golide, ndi ziwiya zina n’kukaziika mosungira chuma cha panyumba ya Yehova.+

  • 1 Mbiri 18:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Zinthu zimenezi Mfumu Davide inazipatulira+ Yehova pamodzi ndi siliva ndi golide amene inalanda ku mitundu yonse,+ kuchokera ku Edomu, ku Mowabu,+ kwa ana a Amoni,+ Afilisiti,+ ndi Aamaleki.+

  • 1 Mbiri 22:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Taona, pa nthawi ya masautso anga+ ndasonkhanitsa golide womangira nyumba ya Yehova wokwanira matalente* 100,000,+ ndi siliva wokwanira matalente 1,000,000. Koma n’zosatheka kuyeza kulemera kwa mkuwa+ ndi zitsulo+ chifukwa n’zochuluka kwambiri. Ndakonzanso matabwa ndi miyala, koma udzawonjezerapo zina.

  • 1 Mbiri 26:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Anayeretsa zinthu zimene anazitenga kunkhondo+ ndiponso zofunkha+ kuti azizigwiritsa ntchito panyumba ya Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena