23 Aroni anatenga Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Naasoni,+ kukhala mkazi wake. Ndipo Eliseba anam’berekera Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+
10Ndiyeno Nadabu ndi Abihu,+ ana a Aroni, aliyense anatenga chofukizira,+ n’kuikamo moto ndi zofukiza+ pamwamba pake. Pamenepo anayamba kupereka zofukiza pamoto wosaloledwa+ ndi Yehova, umene iye sanawalamule.