12 Pamenepo Alevi+ anaimirira. Alevi ake anali Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya ochokera mwa ana a Kohati.+ Kuchokera mwa ana a Merari,+ panali Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli. Kuchokera mwa Agerisoni+ panali Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa.