Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 19:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 “‘Musatembenukire kwa olankhula ndi mizimu+ ndipo musafunsire olosera zam’tsogolo+ ndi kudetsedwa nawo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

  • Levitiko 20:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “‘Munthu wotembenukira kwa olankhula ndi mizimu+ ndi olosera zam’tsogolo,+ komwe n’kuchita mosakhulupirika kwa ine,* ndidzam’kana ndithu ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+

  • 1 Samueli 28:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pamapeto pake, Sauli anauza atumiki ake kuti: “Ndifufuzireni mkazi waluso polankhula ndi mizimu,+ ndipo ine ndipita kukalankhula naye.” Pamenepo atumiki ake anamuuza kuti: “Ku Eni-dori alipo mkazi waluso polankhula ndi mizimu.”+

  • Yesaya 8:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Akakuuzani anthu inu kuti: “Funsirani kwa anthu olankhula ndi mizimu+ kapena kwa anthu amene ali ndi mzimu wolosera zam’tsogolo, omwe amalira ngati mbalame+ ndiponso amalankhula motsitsa mawu,” kodi mtundu uliwonse wa anthu suyenera kufunsira kwa Mulungu wake?+ Kodi tizifunsira kwa anthu akufa kuti athandize anthu amoyo?+

  • Machitidwe 16:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ndiyeno pamene tinali kupita kumalo opempherera, tinakumana ndi mtsikana wina wantchito wogwidwa ndi mzimu,+ chiwanda cholosera zam’tsogolo.+ Iye anali kupezera mabwana ake phindu lochuluka+ mwa kumachita zoloserazo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena