Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 22:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “Mkazi wamatsenga musam’lole kukhala ndi moyo.+

  • Levitiko 19:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 “‘Musatembenukire kwa olankhula ndi mizimu+ ndipo musafunsire olosera zam’tsogolo+ ndi kudetsedwa nawo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

  • Levitiko 20:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “‘Munthu wotembenukira kwa olankhula ndi mizimu+ ndi olosera zam’tsogolo,+ komwe n’kuchita mosakhulupirika kwa ine,* ndidzam’kana ndithu ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+

  • 1 Samueli 15:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Pakuti kupanduka+ n’chimodzimodzi ndi tchimo la kuwombeza,+ ndipo kuchita zinthu modzikuza n’chimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga ndiponso aterafi.+ Popeza iwe wakana mawu a Yehova,+ iyenso wakukana kuti usakhalenso mfumu.”+

  • 1 Samueli 28:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Tsopano Samueli anali atamwalira ndipo Aisiraeli anali atamulira ndi kumuika m’manda mumzinda wakwawo ku Rama.+ Ndipo Sauli anali atachotsa anthu olankhula ndi mizimu ndi akatswiri olosera zam’tsogolo m’dzikolo.+

  • Yesaya 8:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Akakuuzani anthu inu kuti: “Funsirani kwa anthu olankhula ndi mizimu+ kapena kwa anthu amene ali ndi mzimu wolosera zam’tsogolo, omwe amalira ngati mbalame+ ndiponso amalankhula motsitsa mawu,” kodi mtundu uliwonse wa anthu suyenera kufunsira kwa Mulungu wake?+ Kodi tizifunsira kwa anthu akufa kuti athandize anthu amoyo?+

  • Aheberi 3:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Chenjerani abale, kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo n’kukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena