9 Chongofunika n’chakuti musam’pandukire Yehova.+ Komanso anthu a m’dzikolo musawaope,+ chifukwa ali ngati chakudya kwa ife. Alibenso chitetezo,+ koma ifeyo Yehova ali nafe.+ Musawaope ayi.”+
2 Chotero iye anapita kukaonekera kwa Asa n’kumuuza kuti: “Tamverani mfumu Asa ndi anthu onse a fuko la Yuda ndi Benjamini. Yehova akhala nanu inuyo mukapitiriza kukhala naye.+ Mukamufunafuna+ iye adzalola kuti mum’peze, koma mukamusiya nayenso adzakusiyani.+