25 Asilikaliwo atachoka (popeza anamusiya akuvutika kwambiri),+ atumiki ake anam’konzera chiwembu+ chifukwa cha magazi+ a ana a wansembe Yehoyada+ ndipo anamuphera pabedi+ lake. Kenako anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide+ koma sanamuike m’manda a mafumu.+
27 Pomalizira pake, Ahazi anagona pamodzi ndi makolo ake ndipo anaikidwa m’manda mumzinda, ku Yerusalemu. Iye sanaikidwe m’manda a mafumu a Isiraeli.+ Kenako Hezekiya mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.