10 “Ndani pakati panu amene angatseke zitseko za kachisi popanda malipiro?+ Anthu inu mumayatsa moto paguwa langa lansembe kuti mulandire malipiro.+ Ine sindikukondwera nanu, ndipo nsembe zanu zimene mukupereka monga mphatso sizikundisangalatsa,”+ watero Yehova wa makamu.