19 Anafa chifukwa cha machimo ake amene anachita mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndiponso mwa kuyenda m’njira ya Yerobowamu ndi m’tchimo limene iyeyo anachita mwa kuchimwitsa Isiraeli.+
4 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova monga anachitira a m’nyumba ya Ahabu, chifukwa iwowo anakhala alangizi+ ake pambuyo pa imfa ya bambo ake, ndipo anam’pweteketsa.