Deuteronomo 32:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Iwo anali kupereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+Anapereka nsembe kwa milungu imene sanaidziwe,+Milungu yatsopano yongobwera kumene,+Imene makolo anu akale sanaidziwe. 1 Mafumu 12:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Choncho mfumuyo inakambirana ndi anthu ena+ n’kupanga ana awiri a ng’ombe agolide.+ Itatero inauza anthuwo kuti: “N’zovuta kwambiri kwa inu kuti muzipita ku Yerusalemu. Nayu Mulungu wanu+ Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+ 2 Mbiri 11:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Iye anadziikira ansembe m’malo okwezeka+ kuti azitumikira ziwanda zooneka ngati mbuzi*+ ndi mafano a ana a ng’ombe amene iye anapanga.+ Hoseya 8:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Iwe Samariya, fano lako la mwana wa ng’ombe latayidwa.+ Mkwiyo wanga wayakira anthu ako.+ Kodi iwo adzalephera kudziyeretsa ku tchimo lawoli mpaka liti?+
17 Iwo anali kupereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+Anapereka nsembe kwa milungu imene sanaidziwe,+Milungu yatsopano yongobwera kumene,+Imene makolo anu akale sanaidziwe.
28 Choncho mfumuyo inakambirana ndi anthu ena+ n’kupanga ana awiri a ng’ombe agolide.+ Itatero inauza anthuwo kuti: “N’zovuta kwambiri kwa inu kuti muzipita ku Yerusalemu. Nayu Mulungu wanu+ Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+
15 Iye anadziikira ansembe m’malo okwezeka+ kuti azitumikira ziwanda zooneka ngati mbuzi*+ ndi mafano a ana a ng’ombe amene iye anapanga.+
5 Iwe Samariya, fano lako la mwana wa ng’ombe latayidwa.+ Mkwiyo wanga wayakira anthu ako.+ Kodi iwo adzalephera kudziyeretsa ku tchimo lawoli mpaka liti?+