33 Yerobowamu anapereka nsembe pa tsiku la 15, m’mwezi wa 8 womwe anausankha yekha.+ Anapereka nsembezo paguwa limene anamanga ku Beteli. Ndipo anakonzera chikondwerero ana a Isiraeli ndi kupereka nsembe zautsi kuti afukize paguwalo.+
33 Pambuyo pa zimenezi, Yerobowamu sanasiyebe njira yake yoipa. Iye anapitiriza kuika anthu wamba kukhala ansembe a malo okwezeka.+ Aliyense wofuna unsembewo, iye anali kum’patsa mphamvu+ mwa kunena kuti: “Uyu akhale wansembe wa malo okwezeka.”