14 Yehova analimbikitsa+ Zerubabele mwana wa Salatiyeli bwanamkubwa wa Yuda, Yoswa+ mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe ndi anthu ena onse. Choncho iwo anapita kukagwira ntchito panyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wawo.+
7 Ngakhale pataikidwa chopinga chachikulu ngati phiri+ pamaso pa Zerubabele,+ chidzasalazidwa kukhala malo athyathyathya. Ndithu iye adzabweretsa mwala wotsiriza wa pakona.+ Akadzatero anthu adzafuula+ kuti: “Koma mwalawu ndiye ndi wokongola bwanji! Koma ndiye ndi wokongola!”’”+