2 Panali pa nthawi imeneyi pamene Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ananyamuka n’kuyamba kumanganso nyumba ya Mulungu. Nyumbayi inali ku Yerusalemu ndipo panali aneneri a Mulungu+ omwe anali kuwathandiza.
21 akukonzekeretseni ndi chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake. Ndipo kudzera mwa Yesu Khristu, achite mwa ife zimene zili zokondweretsa pamaso pake.+ Kwa iye kukhale ulemerero kwamuyaya.+ Ame.